Psalms 89:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kale mudalankhula m'masomphenya kwa anthu anu okhulupirika, mudati, “Ndamuveka chisoti chaufumu munthu amene ali wamphamvu, ndamukweza amene ali wosankhidwa pakati pa anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo munalankhula m'masomphenya ndi okondedwa anu, ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa chiphona; ndakweza wina wosankhika mwa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kale munayankhula mʼmasomphenya, kwa anthu anu okhulupirika munati, “Ndapatsa mphamvu wankhondo; ndakweza mnyamata wochokera pakati pa anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo munalankhula m'masompenya ndi okondedwa anu, Ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa ciphona; Ndakweza wina wosankhika mwa anthu.