Psalms 89:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chikondi chanu chosasinthika chakhazikika kuti chikhale mpaka muyaya, kukhulupirika kwanu nkwachikhalire ngati mlengalenga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndinati, Chifundo adzachimanga kosaleka; mudzakhazika chikhulupiriko chanu m'Mwamba mwenimweni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzalalikira kuti chikondi chanu chidzakhazikika mpaka muyaya, kuti Inu munakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba kwenikweniko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndinati, Cifundo adzacimanga kosaleka; Mudzakhazika cikhulupiriko canu m'Mwamba mweni mweni.