Psalms 9:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Muti-Labeni. Salimo la Davide. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse; ndidzawerengera zodabwitsa zanu zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a nyimbo ya “Imfa ya Mwana.” Salimo la Davide. Ine ndidzakutamandani, Inu Yehova, ndi mtima wanga wonse; ndidzafotokoza za zodabwitsa zanu zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse; Ndidzawerengera zodabwiza zanu zonse.