Psalms 9:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mwatsimikiza kusalakwa kwanga. Mwakhala pa mpando woweruza, mwagamula kuti ndine wosapalamula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mwandiweruzira mlandu wanga; mwakhala pa mpando wachifumu, woweruza wolungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Inu mwatsimikiza za kulungama kwanga ndi mlandu wanga; Inu mwakhala pa mpando wanu waufumu, kuweruza mwachilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mwandiweruzira mlandu wanga; Mwakhala pa mpando wacifumu, Woweruza wolungama.