Psalms 90:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zaka za moyo wathu nzokwanira makumi asanu ndi aŵiri, tikakhala amphamvu, ndiye makumi asanu ndi atatu. Koma zaka zonsezo ndi za nkhaŵa ndi mavuto. Zakazo zimatha msanga, ife nkumapita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchuluka kwa masiku athu ndi 70, kapena 80 ngati tili ndi mphamvu; komabe zaka zonsezi ndi za mavuto ndi nkhawa, zimatha mofulumira ndipo ife timawulukira kutali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, Kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; Koma teronso kukula kwao kumati cibvuto ndi copanda pace; Pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.