Psalms 90:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tidzazeni m'maŵa mulimonse ndi chikondi chanu chosasinthika, kuti tizikondwa ndi kusangalala masiku athu onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mutikhutitse nacho chifundo chanu m'mawa; ndipo tidzafuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mutikhutitse mmawa ndi chikondi chanu chosatha, kuti tiyimbe ndi chimwemwe ndi kukhala okondwa masiku athu onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mutikhutitse naco cifundo canu m'mawa; Ndipo tidzapfuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.