Psalms 91:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa; ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; Ndidzamkweza m'mwamba, papeza adziwa dzina langa.