Psalms 95:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo, choncho ndidati, “Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika, sasamalako njira zanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa zaka makumi anayi ndinali wokwiya ndi mʼbado umenewo; ndipo ndinati, “Iwo ndi anthu amene mitima yawo imasochera ndipo sanadziwe njira zanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa cisoni, Ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, Ndipo sadziwa njira zanga.