Psalms 98:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wakumbukira chikondi chake chosasinthika ndi kukhulupirika kwake pa fuko la Israele. Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anakumbukira chifundo chake ndi chikhulupiriko chake kunyumba ya Israele; malekezero onse a dziko lapansi anaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye wakumbukira chikondi chake ndi kukhulupirika kwake pa Aisraeli; malekezero onse a dziko lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anakumbukila cifundo cace ndi cikhulupiriko cace ku nyumba ya Israyeli; Malekezero onse a dziko lapansi anaona cipulumutso ca Mulungu wathu.