Psalms 99:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose ndi aroni anali ena mwa ansembe ake, Samuele nayenso anali mmodzi mwa anthu otama dzina la Chauta mopemba. Ankalira kwa Chauta Iye nkumaŵayankha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake, Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake; iwo anayitana Yehova ndipo Iyeyo anawayankha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa ansembe ace muli Mose ndi Aroni, Ndi Samueli mwa iwo akuitanira dzina lace; Anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.