Revelation 1:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Liwulo lidati, “Zimene ukuwonazi, uzilembe m'buku ndipo ulitumize kwa mipingo isanu ndi iŵiri iyi: wa ku Efeso, wa ku Smirina, wa ku Pergamo, wa ku Tiatira, wa ku Sardi, wa ku Filadelfiya ndi wa ku Laodikea.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuti, Chimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smirina, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiatira, ndi ku Sardi, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikea.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
amene anati, “Lemba mʼbuku zimene ukuziona ndipo uzitumize ku mipingo isanu ndi iwiri ya ku Efeso, Simurna, Pergamo, Tiyatira, Sarde, Filadefiya ndi ku Laodikaya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuti, Cimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smurna, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiyatira, ndi ku Sarde, ndi ku Filadelfeya, ndi ku Laodikaya.