Revelation 1:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'dzanja lake lamanja adaanyamula nyenyezi zisanu ndi ziŵiri, ndipo m'kamwa mwake munali lupanga lakuthwa konsekonse lotulukira kunja. Nkhope yake inali yoŵala ngati dzuŵa lamasana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m'kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼdzanja lake lamanja ananyamula nyenyezi zisanu ndi ziwiri, ndipo mʼkamwa mwake munali lupanga lakuthwa konsekonse. Nkhope yake imawala ngati dzuwa lowala kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'dzanja lace lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwirl; ndi m'kamwa mwace mudaturuka lupanga lakuthwa konse konse; ndipo nkhope yace ngati dzuwa lowala mu mphamvu yace.