Revelation 1:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zija zimene waziwona m'dzanja langa lamanja, ndi china chija cha ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide, tanthauzo lake ndi ili: Nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zija ndi atsogoleri a mipingo isanu ndi iŵiri; ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zija ndi mipingo isanu ndi iŵiri imene.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona pa dzanja langa lamanja, ndi zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tanthauzo la nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene waziona mʼdzanja langa lamanja ndi la zoyikapo nyale zagolide zisanu ndi ziwiri ndi ili: Nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndi angelo a mipingo isanu ndi iwiri ija, ndipo zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zija ndi mipingo isanu ndi iwiri ija.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
3 cinsinsi ca nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona pa dzanja langa lamanja, ndi 4 zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo 5 angelo a Mipingo isanu ndi iwirl; ndipo zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri ndizo 6 Mipingo isanu ndi iwiri.