Revelation 1:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndine, Yohane, ndikulembera mipingo isanu ndi iŵiri ya ku Asiya. Akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere Mulungu amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza. Ikukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere mizimu isanu ndi iŵiri yokhala patsogolo pa mpando wachifumu wa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yohane kwa Mipingo isanu ndi iwiri m'Asiya: Chisomo kwa inu ndi mtendere, zochokera kwa Iye amene ali, ndi amene adali, ndi amene alinkudza; ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala kumpando wachifumu wake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndine Yohane, Kupita ku mipingo isanu ndi iwiri ya mʼchigawo cha Asiya. Chisomo ndi mtendere kwa inu, kuchokera kwa Iye amene ali, amene analipo ndi amene akubwera ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala patsogolo pa mpando wake waufumu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yohane kwa Mipingo isanu ndi wiri m'Asiya: Cisomo kwa inu ndi ntendere, zocokerakwa iye amene ili, ndi amene adali, ndi amene aliikudza; ndi kwa mizimu isanu ndi wiri yokhala ku mpando wacifumu vace;