Revelation 1:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adatisandutsa mafumu, kuti tizitumikira Mulungu Atate ake modzipereka ngati mtundu wa ansembe. Motero Yesu Khristuyo alandire ulemerero ndi mphamvu zolamulira mpaka muyaya. Amen.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi. Amen.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo watisandutsa mafumu ndi ansembe kuti tizitumikira Mulungu ndi Atate ake. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu ku nthawi zosatha, Ameni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wace; kwa iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi. Amen.