Revelation 10:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera Kumwamba. Adaavala mtambo, ndipo pozungulira mutu wake panali utawaleza. Nkhope yake inali ngati dzuŵa, miyendo yake ngati mizati yamoto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona mngelo wina wolimba alikutsika Kumwamba, wovala mtambo; ndi utawaleza pamutu pake, ndi nkhope yake ngati dzuwa, ndi mapazi ake ngati mizati yamoto;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera kumwamba. Anavala mtambo ndipo anali ndi utawaleza pamutu pake. Nkhope yake inali ngati dzuwa, ndipo miyendo yake inali ngati mizati yamoto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona mngelo wina wolimba alikutsika Kumwamba, wobvala mtambo; ndi utawaleza pamutu pace, ndi nkhope yace ngati dzuwa, ndi mapazi ace ngati mizati yamoto;