Revelation 10:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mabinguwo atangogunda, ndidaati ndilembe. Koma ndidamva mau ochokera Kumwamba akuti, “Zisunge mu mtima zimene mabingu asanu ndi aŵiri aja anena. Usazilembe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene adalankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndinati ndilembe; ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba nanena, Sindikiza nacho chizindikiro zimene adalankhula mabingu asanu ndi awiri, ndipo usazilembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mabingu asanu ndi awiriwo atangogunda, ine ndinkati ndizilemba; koma ndinamva mawu kuchokera kumwamba kuti, “Zisunge mu mtima zimene mabingu asanu ndi awiriwo anena ndipo usazilembe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene adalankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndinati ndilembe; ndipo udinamva mau ocokera Kumwamba nanena, Sindikiza naco cizindikilo zimene adalankhula mabingu asanu ndi limodzi, ndipo usazilembe,