Revelation 10:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatero adalumbira m'dzina la Mulungu wokhala ndi moyo mpaka muyaya, amene adalenga thambo lakumwamba ndi zonse zokhala kumeneko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo, ndiponso nyanja ndi zonse zokhala m'menemo. Mngeloyo kulumbira kwake adati, “Pasakhalenso zochedwa tsopano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nalumbira kutchula Iye amene ali ndi moyo kunthawi za nthawi, amene analenga m'mwamba ndi zinthu zili momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu zili momwemo, ndi nyanja ndi zinthu zili momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngeloyo analumbira mʼdzina la Iye wokhala ndi moyo mpaka muyaya, amene analenga kumwamba ndi zonse zili kumeneko, dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo, nati, “Pasakhalenso zochedwa tsopano!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nalumbira kuchula iye amene ali ndi moyo ku nthawi za nthawi, amene analenga m'mwamba ndi zinthu ziri momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu ziri momwemo, ndi nyanja ndi zinthu ziri momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi: