Revelation 10:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo mau amene ndidaamva kuchokera Kumwamba adandilankhulanso, adati, “Pita, katenge kampukutu kofutukula kaja kamene kali m'manja mwa mngelo woponda pa nyanja ndi pa mtunda uja.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mau ndinawamva ochokera Kumwamba, analankhulanso nane, nanena, Muka, tenga buku lofunyululalo m'dzanja la mngelo wakuimirira panyanja ndi padziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mawu amene ndinamva kuchokera kumwamba aja, anandiyankhulanso, anati, “Pita katenge buku lotsekulidwalo mʼdzanja la mngelo amene waponda pa nyanja ndi pa mtundayo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mau ndinawamva ocokera Kumwamba, analankhulanso nane, nanena, Muka, tenga buku lofunyululalom'dzanja la mngelo wakuimirira panyanja ndi padziko.