Revelation 10:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidapitadi kwa mngeloyo nkumupempha kuti andipatse kampukutuko. Iye adati, “Kwaya, idya. M'mimba mwako kaziŵaŵa, koma m'kamwa mwako kazizuna ngati uchi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinamuka kwa mngelo, ndi kunena naye, Ndipatse kabukuko. Ndipo ananena ndi ine, Dzatenge, nudye; ndipo kadzawawitsa m'mimba mwako, komatu m'kamwa mwako kadzazuna ngati uchi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ndinapita kwa mngeloyo ndipo ndinamupempha kuti andipatse kabukuko. Iye anati, “Tenga, idya. Mʼmimba mwako kaziwawa koma mʼkamwa mwako kazizuna ngati uchi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinamuka kwa mngelo, ndi kunena naye, Ndipatse kabukuko. Ndipo ananena ndi ine, Dzatenge, nudye; ndipo kadzawawitsa m'mimbamwako, komatu m'kamwa mwako kadzazuna ngati uci.