Revelation 11:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiŵiri adaliza lipenga lake. Atatero kumwamba kudamveka mau okweza. Mauwo adati, “Tsopano mphamvu zolamulira dziko lapansi zili m'manja mwa Ambuye athu ndi mwa Wodzozedwa wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau akulu m'Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wachisanu ndi chiwiri anawomba lipenga lake, ndipo kumwamba kunamveka mawu ofuwula amene anati, “Ufumu wa dziko lapansi uli mʼmanja mwa Ambuye athu ndi Khristu wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mngelo wacisanu ndi ciwiri anaomba, ndipo panakhala mau akulu m'Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wace: ndipo adzacita ufumu kufikira nthawi za nthawi.