Revelation 11:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu akunja adakalipa, koma yafika nthaŵi yoonetsa mkwiyo wanu, ndiye kuti nthaŵi yoweruza anthu akufa. Yafika nthaŵi yoti mupereke mphotho kwa atumiki anu, aneneri, ndi kwa anthu anu, ndiye kuti onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu, amene amaopa dzina lanu. Yafika nthaŵi yoti muŵaononge amene akuwononga dziko lapansi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang'ono ndi akulu; ndi kuononga iwo akuononga dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
A mitundu ina anapsa mtima; koma yafika nthawi yoonetsa mkwiyo. Nthawi yakwana yoweruza anthu akufa, yopereka mphotho kwa atumiki anu, aneneri, anthu oyera mtima anu ndi amene amaopa dzina lanu, wamngʼono pamodzi ndi wamkulu yemwe. Yafika nthawi yowononga amene awononga dziko lapansi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang'ono ndi akuru; ndi kuononga iwo akuononga dziko.