Revelation 11:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a mitundu yonse, a mafuko onse ndiponso a zilankhulo zonse azidzayang'anitsitsa mitemboyo masiku atatu ndi hafu, akukana kuti iikidwe m'manda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo a mwa anthu ndi mafuko, ndi manenedwe, ndi mitundu apenyera mitembo yao masiku atatu ndi nusu lake, osalola mitembo yao iikidwe m'manda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa masiku atatu ndi theka, anthu ochokera ku mtundu uliwonse, fuko lililonse, chiyankhulo chilichonse ndi dziko lililonse, azidzayangʼanitsitsa mitembo yawoyo koma adzakana kuyikwirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo a mwa anthu ndi mafuko, ndi manenedwe, ndi mitundu apenyera mitembo yao masiku atatu ndi nusu lace, osalola mitembo yao iikidwe m'manda.