Revelation 12:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo ndidamva mau amphamvu Kumwamba akunena kuti, “Tsopano Mulungu wathu watipulumutsa. Waonetsa mphamvu zake ndi ufumu wake. Tsopano Wodzozedwa uja waonetsa ulamuliro wake. Woneneza abale athu uja wagwetsedwa pansi, amangokhalira kuŵaneneza kwa Mulungu wathu usana ndi usiku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinamva mau akulu m'Mwamba, nanena, Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinamva mawu ofuwula kumwamba akunena kuti, “Tsopano chipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu ndi ulamuliro wa Khristu wake zabwera. Pakuti woneneza abale athu uja, amene amangokhalira kuwaneneza pamaso pa Mulungu usana ndi usiku, wagwetsedwa pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinamva mau akuru m'Mwamba, nanena, Tsopano zafika cipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wace; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.