Revelation 12:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma maiyo adapatsidwa mapiko aŵiri a chiwombankhanga chachikulu kuti athaŵire ku malo ake aja akuchipululu. Kumeneko adzasamalidwa zaka zitatu ndi hafu, kuwopa kuti chinjoka chija chingamuwone.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a chiombankhanga chachikulu, kuti akaulukire kuchipululu, ku mbuto yake, kumene adyetsedwako nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayiyo anapatsidwa mapiko awiri a chiwombankhanga chachikulu kuti athawire ku malo ake aja a ku chipululu. Kumeneko adzasamalidwako zaka zitatu ndi theka kuti chinjoka chija chisamupeze.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a ciombankhanga cacikuru, kuti akaulukire kucipululu, ku mbuto yace, kumene adyetsedwako nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka.