Revelation 12:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma dziko lapansi lidamthandiza maiyo: lidayasama nkuumeza mtsinje umene chinjoka chija chidaalavula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dziko linathandiza mkaziyo, ndi dziko linatsegula m'kamwa mwake, nilinameza madzi a mtsinje amene chinjoka chinalavula m'kamwa mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma dziko lapansi linamuthandiza mayiyo. Nthaka inatsekuka ndi kumeza mtsinje uja unachokera mʼkamwa mwa chinjokacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dziko linathandiza mkaziyo, ndi dziko linatsegula m'kamwa mwace, nilinameza madzi a mtsinje amene cinjoka cinalabvula m'kamwamwace.