Revelation 12:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi mchira wake chidakokolola chimodzi mwa zigawo zitatu za nyenyezi zakuthambo, nkuzigwetsa pa dziko lapansi. Chinjokacho chidadzaimirira pamaso pa mai uja amene anali pafupi kubala mwana, kuti akangobadwa mwanayo, chimudye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mchira wake uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo chinjoka chinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala icho chikalikwire mwana wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mchira wake unakokolola gawo limodzi la magawo atatu a nyenyezi kuzichotsa ku thambo ndi kuziponya pa dziko lapansi. Chinjoka chija chinadzayima patsogolo pa mayi uja amene anali pafupi kuberekayu kuti mwanayo akangobadwa chimudye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mcira wace uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo cinjoka cinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala, ico cikalikwire mwana wace.