Revelation 12:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chinjoka chachikulu chija chidagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakale ija yotchedwa “Mdyerekezi” ndiponso “Satana”, wonyenga anthu a pa dziko lonse lapansi. Chidagwetsedwa pa dziko lapansi pamodzi ndi angelo ake onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chinjoka chachikulu chija chinagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakalekale ija yotchedwa Mdierekezi kapena Satana, amene amasocheretsa anthu a pa dziko lonse lapansi. Chinaponyedwa pa dziko la pansi pamodzi ndi angelo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cinaponyedwa pansi cinjoka cacikuru, njoka yokalambayo, iye wochedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; cinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ace anaponyedwa naye pamodzi.