Revelation 13:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidaona chilombo chikuvuuka m'nyanja. Chinali ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iŵiri. Pa nyanga iliyonse chidaavala chisoti chaufumu, ndipo pa mutu uliwonse panali dzina lonyoza Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaimirira pa mchenga wa nyanja. Ndipo ndinaona chilombo chilinkutuluka m'nyanja, chakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ndi iwiri, ndi pa nyanga zake nduwira zachifumu khumi, ndi pamitu pake maina a mwano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinaona chirombo chikutuluka mʼnyanja. Chinali ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iwiri. Pa nyanga iliyonse chinavala chipewa chaufumu, ndipo pa mutu uliwonse panali dzina lonyoza Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaimirira pa mcenga wa nyanja. Ndipo ndinaona cirombo cirinkuturuka m'nyanja, cakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ow iwiri, ndi pa nyanga zace nduwira zacifumu khumi, ndi pamitu pace maina a mwano.