Revelation 13:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Woyenera kutengedwa ku ukapolo, kuukapoloko akapitadi. Woyenera kuphedwa ku nkhondo, kunkhondoko akaphedwadi. Pamenepa ndiye pamene anthu a Mulungu ayenera kuwonetsa kupirira ndi kulimbika m'chikhulupiriro.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati munthu alinga kundende, kundende adzamuka; munthu akapha ndi lupanga, ayenera iye kuphedwa nalo lupanga. Pano pali chipiriro ndi chikhulupiriro cha oyera mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Woyenera kupita ku ukapolo, adzapita ku ukapolo. Woyenera kufa ndi lupanga, adzafa ndi lupanga.” Pamenepa kwa anthu a Mulungu pakufunika kupirira ndi kukhulupirika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
N gati munthu alinga kundende, kundende adzamuka munthu akapha ndi lupanga, ayenera iyekuphedwa nalo lupanga, Pano pali cipiriro ndi cikhulupiriro ca oyera mtima.