Revelation 13:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka ndidaona chilombo china chikutuluka pansi. Chinali ndi nyanga ziŵiri ngati mwanawankhosa, kulankhula kwake ngati kwa chinjoka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona chilombo china chilikutuluka pansi; ndipo chinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwanawankhosa, ndipo chinalankhula ngati chinjoka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinaona chirombo china chikutuluka mʼnthaka. Chinali ndi nyanga ziwiri ngati mwana wankhosa koma kuyankhula kwake ngati chinjoka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona cirombo cina cirikuturuka pansi; ndipo cinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwana wa nkhosa, ndipo cinalankhula ngati cinjoka.