Revelation 13:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chinkalamulira pamaso pa chilombo choyamba chija ndi mphamvu zimene chilombo choyambacho chidaachipatsa. Chinkakakamiza dziko lapansi ndi onse okhalamo kuti azipembedza chilombo choyamba chija chimene bala lake lofa nalo lija linali litapola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chichita ulamuliro wonse wa chilombo choyamba pamaso pake. Ndipo chilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo chilombo choyamba, chimene bala lake la kuimfa lidapola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chinalamulira ndi mphamvu zonse za chirombo choyamba chija, ndipo chinachititsa kuti dziko lapansi ndi anthu okhalamo alambire chirombo choyamba chija, chimene bala lake losati nʼkupola linali litapola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cicita ulamuliro wonse wa cirombo coyamba pamaso pace. Ndipo cilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo cirombo coyamba, cimene bala lace la kuimfa lidapola.