Revelation 13:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chinkanyenganso anthu okhala pa dziko lapansi ndi zozizwitsa zimene chidaaloledwa kuchita pamaso pa chilombo choyamba chija. Chinkauza anthu okhala pa dziko lapansiwo kuti apange fano lolemekezera chilombo chimene chidaavulazidwa ndi lupanga, koma nkukhalabe moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga nichinakhalanso ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha zizindikiro zimene chinaloledwa kuchita mʼmalo mwa chirombo choyamba chija, chimene bala lake linapola, chinanyenga anthu okhala pa dziko lapansi. Chinalamula anthu kuti apange fano mopereka ulemu kwa chirombo chimene chinavulazidwa ndi lupanga, koma nʼkukhalabe ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikilo zimene anacipatsa mphamvu yakuzicita pamaso pa cirombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fane la ciromboco, cimene cinali nalo bala la lupanga nicinakhalanso ndi moyo.