Revelation 13:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chilombo chimene ndidaaonacho chinali ngati kambuku, mapazi ake ngati a chimbalangondo, kukamwa kwake ngati kwa mkango. Chinjoka chija chidaapatsa chilombocho mphamvu zake, mpando wake wachifumu, ndiponso ulamuliro waukulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chilombo ndinachionacho chinafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ake ngati mapazi a chimbalangondo, ndi pakamwa pake ngati pakamwa pa mkango; ndipo chinjoka chinampatsa iye mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chirombo chimene ndinachionacho chinali ngati kambuku, mapazi ake ngati chimbalangondo, kukamwa kwake ngati kwa mkango. Chinjoka chija chinapatsa chirombocho mphamvu zake, mpando wake waufumu ndiponso ulamuliro waukulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cirombo ndinacionaco cinafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ace ngati mapazi a fisi, ndi pakamwa pace ngati pakamwa pa mkango; ndipo cinjoka cinampatsa iye mphamvu yace, ndi mpando wacifumu wace, ndi ulamuliro waukuru.