Revelation 13:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Umodzi mwa mitu yake unkaoneka ngati uli ndi bala lofa nalo, koma balalo linali litapola. Pamenepo anthu onse ankachitsata chilombocho ali odabwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo umodzi wa mitu yake unakhala ngati unalasidwa kufikira imfa; ndipo bala lake la kuimfa lidapola; ndipo dziko lonse linazizwa potsata chilombocho;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Umodzi wa mitu wa chirombocho unkaoneka ngati uli ndi bala losati nʼkupola, koma nʼkuti balalo litapola. Dziko lonse linadabwa ndipo linatsatira chirombocho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo umodzi wa mitu yace unakhala ngati unalasidwa kufikira imfa; ndipo bala lace la kuimfa lidapola; ndipo dziko lonse linazizwa potsata ciromboco;