Revelation 13:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adachipembedza chinjoka chija chifukwa chidaapatsa ulamuliro wake kwa chilombo chija. Nachonso chilombo chija adachipembedza nkumanena kuti, “Ndani angafanane ndi chilombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo analambira chinjoka, chifukwa chinachipatsa ulamuliro chilombocho; ndipo analambira chilombo ndi kunena, Afanana ndi chilombo ndani? Ndipo akhoza ndani kugwira nkhondo nacho?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu anapembedza chinjoka chija chifukwa chinapereka ulamuliro wake kwa chirombocho. Nachonso chirombo chija anachipembedza nʼkumafunsa kuti, “Ndani angafanane ndi chirombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo analambira cinjoka, cifukwa cinacipatsa ulamuliro ciromboco; ndipo analambira cirombo ndi kunena, Manana ndi cirombo ndani? Ndipo akhoza ndani kugwira nkhondo naco?