Revelation 13:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse okhala pa dziko lapansi adzachipembedza, ndiye kuti aliyense amene, chilengedwere dziko lapansi, dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo la Mwanawankhosa adaphedwa uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse okhala pa dziko lapansi adzapembedza chirombocho, aliyense amene chilengedwere cha dziko lapansi dzina lake silinalembedwe mʼbuku la amoyo la Mwana Wankhosa anaphedwa uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzacilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi,