Revelation 14:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona Mwanawankhosa ataimirira pa Phiri la Ziyoni. Pamodzi ndi Iye panali anthu zikwi 144, olembedwa dzina lake ndiponso dzina la Atate ake pamphumi pao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira pa phiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinaona patsogolo panga panali Mwana Wankhosa, atayimirira pa Phiri la Ziyoni, ndipo Iye anali pamodzi ndi anthu 144,000 amene pa mphumi pawo panalembedwa dzina la Mwana Wankhosayo ndi la Atate ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira pa phiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lace ndi dzina la Atate wace lolembedwa pamphumi pao.