Revelation 14:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
nayenso adzamwako vinyo wa ukali wa Mulungu. Vinyo wake adzathiridwa, popanda kanthu kochepetsa mphamvu yake, m'chikho cha mkwiyo wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto ndi miyala yasulufure yoyaka. Zimenezi zidzachitikira pamaso pa angelo a Mulungu, ndi Mwanawankhosa uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
iyenso adzamwako kuvinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasanganiza m'chikho cha mkwiyo wake; ndipo adzazunzika ndi moto ndi sulufure pamaso pa angelo oyera mtima ndi pamaso pa Mwanawankhosa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nayenso adzamwa vinyo waukali wa Mulungu, umene wathiridwa popanda kuchepetsa mphamvu zake mʼchikho cha ukali wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto wamiyala yasulufure pamaso pa angelo oyera ndi pa Mwana Wankhosa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
iyenso adzamwako kuvinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasanganiza m'cikho ca mkwiyo wace; ndipo adzazunzika ndi moto ndi sulfure pamaso pa angelo oyera mtima ndi pamaso pa Mwanawankhosa j