Revelation 14:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Utsi wa moto woŵazunzawo umakwera kumwamba mpaka muyaya. Anthu amene adapembedza chilombo chija ndi fano lake, ndiponso amene adalembedwa chizindikiro cha dzina lake chija, sapeza mpumulo usana kapena usiku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo utsi wa kuzunza kwao ukwera kunthawi za nthawi; ndipo sapuma usana ndi usiku iwo akulambira chilombocho ndi fano lake, ndi iye aliyense akalandira lemba la dzina lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo utsi wa moto wowazunzawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya. Sikudzakhala kupumula usana ndi usiku kwa amene anapembedza chirombo chija ndi fano lake kapena kwa aliyense amene analembedwa chizindikiro cha dzina lake lija.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo utsi wa kuzunza kwao tukwera ku nthawiza nthawi; ndipo sapuma usana ndi usiku: iwo akulambira ciromboco ndi fano lace, ndi iye ali yense akalandira lemba la dzina lace.