Revelation 14:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidamva mau ochokera Kumwamba. Adati, “Lemba kuti, Ngodala anthu akufa amene kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo muno afa ali otumikira Ambuye.” Mzimu Woyera akuti, “Inde, ngodaladi. Akapumule ntchito zao zolemetsa, pakuti ntchito zaozo zimaŵatsata.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti ntchito zao zitsatana nao pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinamva mawu kuchokera kumwamba akuti, “Lemba kuti, Odala anthu amene akufa ali mwa Ambuye kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo.” “Inde,” akutero Mzimu, “akapumule ntchito zawo zotopetsa pakuti ntchito zawo zidzawatsata.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinamva mau ocokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti nchito zao zitsatana nao pamodzi.