Revelation 14:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mngelo wina adatuluka m'Nyumba ya Mulungu nafuula ndi mau amphamvu kwa Uja wokhala pamtamboyu. Adati, “Gwiritsa ntchito chikwakwa chako, yambapo kudula dzinthu. Tsopano nyengo yamasika yafika, ndipo dzinthu dza pa dziko lapansi dzidacha kale.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mngelo wina anatuluka m'Kachisi, wofuula ndi mau akulu kwa Iye wakukhala pamtambo, Tumiza chisenga chako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zachetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mngelo wina anatuluka mʼNyumba ya Mulungu nafuwula mwamphamvu kwa uja wokhala pa mtamboyu. Mngeloyo anati, “Tenga chikwakwa chako ndipo kolola, pakuti nthawi yokolola ya dziko la pansi yakwana”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mngelo wina anaturuka m'Kacisi, wopfuulandi mau akuru kwa iye wakukhala pamtambo, Tumiza zenga lako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zacetsa.