Revelation 14:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka mngelo winanso, amene amalamulira moto, adatulukira kuchokera ku guwa lansembe. Adafuula ndi mau amphamvu kwa Uja wokhala ndi chikwakwa chakuthwa. Adati, “Gwiritsa ntchito chikwakwa chakocho, yambapo kudula mphesa za m'munda wamphesa wa pa dziko lapansi, pakuti mphesazo zidapsa kale.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mngelo wina anatuluka pa guwa la nsembe, ndiye wakukhala nao ulamuliro pamoto; nafuula ndi mau akulu kwa iye wakukhala nacho chisenga chakuthwa, nanena, Tumiza chisenga chako chakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m'dziko; pakuti mphesa zake zapsa ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mngelo winanso amene amalamulira moto, anatuluka kuchokera ku guwa lansembe nayitana mwamphamvu mngelo uja amene anali ndi chikwakwa chakunthwa chija, nati, “Tenga chikwakwa chako chakunthwacho yamba kudula mphesa za mʼmunda wamphesa wa pa dziko lapansi, pakuti mphesa zapsa kale.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mngelo wina anaturuka pa guwa la nsembe, ndiye wakukhala nao ulamuliro pamoto; napfuula ndi mau akuru kwa iye wakukhala nalo zenga lakuthwa, nanena, 1 Tumiza zenga lako lakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m'dziko; pakuti mphesa zace zapsa ndithu.