Revelation 14:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidamva liwu lochokera kumwamba longa ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Liwu limene ndidaamvalo linkamveka ngati anthu akuimba azeze ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndi ngati mau a bingu lalikulu; ndipo mau amene ndinawamva anakhala ngati a azeze akuimba azeze ao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinamva liwu lochokera kumwamba ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Liwu limene ndinamvalo linali ngati a anthu akuyimba azeze awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinamva mau ocokera Kumwamba, ngati mkokomo wamadzi ambiri, ndi ngati mau a bingu lalikuru; ndipo mauamene ndinawamva anakhala ngati a azeze akuyimba azeze ao j