Revelation 14:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aja ankaimba nyimbo yatsopano pamaso pa mpando wachifumu uja ndi pamaso pa Zamoyo zinai zija, ndi Akuluakulu aja. Panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kuiphunzira nyimboyo, kupatula anthu zikwi 144 aja amene anali ataomboledwa mu ukapolo wa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo aimba ngati nyimbo yatsopano kumpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimboyi, koma zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kuchokera kudziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwo ankayimba nyimbo yatsopano patsogolo pa mpando waufumu ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kuphunzira nyimboyo kupatula anthu 144,000 aja amene anawomboledwa pa dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ayimba ngati nyimbo yatsopane ku mpando wacifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimboyi, kama zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kucokera kudziko.