Revelation 14:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mngeloyo adanena mokweza mau kuti, “Opani Mulungu ndi kumtamanda, pakuti yafika nthaŵi yoti aweruze anthu. Mumpembedze Iye amene adalenga thambo, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe a madzi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kunena ndi mau akulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga m'mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngeloyo anayankhula mokweza mawu kuti, “Wopani Mulungu ndi kumutamanda, chifukwa nthawi yoweruza anthu yafika. Mumupembedze Iye amene analenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi akasupe amadzi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kunena ndi mau akuru, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya ciweruziro cace; ndipo mlambireni iye amene analenga m'mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi,