Revelation 14:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Padafika mngelo wina wachiŵiri wotsatana ndi woyamba uja. Adati, “Wagwa, wagwa Babiloni wotchuka uja, amene ankamwetsa anthu a mitundu yonse vinyo wa zilakolako zake zadama.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatsata mngelo wina mnzake ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wachiwiri anatsatana naye ndipo anati, “Wagwa! Wagwa Babuloni womveka uja, amene anachititsa anthu a mitundu yonse kumwa vinyo wa zilakolako zake zachigololo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatsata mngelo wina mnzace ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babulo waukuru umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa cigololo cace.