Revelation 15:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidaona Kumwamba chizindikiro china chachikulu ndi chododometsa: angelo asanu ndi aŵiri okhala ndi miliri isanu ndi iŵiri. Miliriyo ndi yotsiriza, pakuti ukali wa Mulungu uthera pa imeneyi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona chizindikiro china m'mwamba, chachikulu ndi chozizwitsa, angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumwamba ndinaona chizindikiro china chachikulu ndi chodabwitsa: angelo asanu ndi awiri ali ndi miliri isanu ndi iwiri yomaliza chifukwa Mulungu anakwiya kotheratu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona cizindikilo cina m'mwamba, cacikuru ndi cozizwitsa, angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu.