Revelation 15:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka ndidaona ngati nyanja ya galasi losanganiza ndi moto. Ndidaonanso anthu amene adapambana chilombo chija, fano lake lija, ndi nambala yotanthauza dzina lake. Anthuwo adaaimirira pamphepete pa nyanja yagalasi ija, m'manjamu ali ndi azeze oŵapatsa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona ngati nyanja yagalasi yosanganiza ndi moto; ndipo iwo amene anachilaka chilombocho, ndi fano lake ndi chiwerengero cha dzina lake, anaimirira pa nyanja yagalasi, nakhala nao azeze a Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinaona chimene chinaoneka ngati nyanja yonyezimira yosakaniza ndi moto, ndipo pambali pa nyanjayo panayima amene anagonjetsa chirombo chija ndi fano lake, ndi nambala yotanthauza dzina lake. Anthuwo ananyamula azeze amene Mulungu anawapatsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona ngati nyanja yamandala yosanganiza ndi moto; ndipo iwo amene anaeilaka ciromboco, ndi fano lace ndi ciwerengero ca dzina lace, anaimirira pa nyanja ya mandala, nakhala nao azeze a Mulungu.