Revelation 15:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankaimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa uja. Mau ake ankati, “Ambuye, Mulungu Mphambe, ntchito zanu nzazikulu ndi zododometsa. Inu, Mfumu ya anthu a mitundu yonse, njira zanu nzolungama ndi zoona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo ankayimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwana Wankhosa. Nyimbo yake inkati, “Zochita zanu ndi zazikulu ndi zodabwitsa, Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse Njira zanu ndi zachilungamo ndi zoona, Mfumu ya mitundu yonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ayimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Nchito zanu nzazikuru ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.